Breaking News:

News

MAKOPONI ATHETSEDWA – Alimi ochuluka apindula ndi ndondomeko ya zipangizo za ulimi zotsika mtengo

0

Boma la Malawi kudzera mu Unduna wa za ulimi lathetsa ndondomeko yoti alimi azigula zipangizo za ulimi zotsika mtengo pogwiritsa ntchito makoponi ndipo labweretsa ndondomeko ya tsopano yomwe alimi sazigwiritsanso ntchito makoponi wa.

Polankhula pa mkumano omwe nduna ya za ulimi a Lobin Lowe inali nawo ndi aphungu a nyumba ya malamulo a mu komiti yoona za ulimi lachitatu mu mzinda wa Lilongwe, ndunayi inatsindikira makosana ndi makosakaziwa kuti boma lakozeka mokwanira kukwaniritsa zomwe zili mu ndondomeko ya tsopanoyi.

A Lowe anaonjezera ndi kunena kuti unduna wawo wakozeka kufikira alimi pafupifupi 4.2 miliyoni ndipo banja lirilonse lidzaloredwa kugula Matumba awiri a feteleza omwe limodzi ndi la fetereza okulitsa mbewu ndinso thumba limodzi la fetereza obereketsa komanso mbewu ya chimanga kapena mpunga yosachepera 5 kilogalamu.

“Tathetsa makoponi chifukwa ndondomeko imeneyi imangopindulira anthu ochepa kobasi ndipo tabweretsa ndondomeko ya tsopano yomwe m’limi sazigawananso ndi wina fetereza yemwe azigula pa mtengo wa K4495 pogwiritsa ntchito chiphaso cha unzika.” umu ndi m’mene ndunayi inanenera.

Ndunayi inaonjezera ndi kunena kuti ndi cholinga cha mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera kuonetsetsa kuti Ulemu wa Mafumu ubwelere pozindikira kuti ndondomeko ya makoponi imachotsa ulemu wa Mafumu makamaka pa kasankhidwe ka anthu oti apindule ndi makoponi ndipo ndondomeko ya tsopanoyi ifikira alimi onse ang’onoang’ono omwe ndi 4.2 miliyoni.

Nthumwi za ku nyumba ya malamulo I nazo zinasonyeza kukhutitsidwa ndi ndondomeko ya tsopanoyi ndipo zapempha unduna wa za malimidwewu kuti uwonetsetse kuti njira zonse za katangale zomwe zimasokoneza ndondomeko zabwino ngati izi zatsekedwa bwino lomwe ndicholinga choti ndondomekoyi ipinduliredi anthu ovutika kuti nawonso akwanitse kukhala ndi chakudya chowakwanira pa mawanja awo.

Pothirirapo mulomo pa langizoli, a Lowe anatsindika kuti unduna wawo ugwira ntchito ndi a bungwe lolemba zika za dziko lomwe limapereka ziphaso za uzika, apolisi ochuluka komanso akazitape a boma omwe athandizire kuonetsetsa kuti katangale wa mtundu wina uliwonse usachitike ndipo iwo anenetsa kuti yemwe atagwidwe akuchita zakatangale, adzalangidwa koopsa.

Boma la Malawi limadalira ulimi ndipo anthu oposa 80 pa anthu 100 aliwonse, moyo wawo umadalira ulimi.

Related Posts

Leave a reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

 • Mrs Mia inspires DPP senior officials

  In a leaked whatsapp conversation among DPP gurus the blue officials said they wish Mrs Abida Mia who has a hardworking spirit was in their team. The DPP officials which include; Ben Phiri, Ngeme Kalilani and Nicholas Dausi just to mention a few said Abida Mia is an insiration to all women in politics. One…

 • Govt withdrawals Vice President’s security detail 

  By Feston Malekezo/ Times Media Malawi Government has withdrawn the Vice President Saulos Chilima’s security detail with immediate effect, the office of the vice president said late Wednesday. “It’s true that today we were informed that the Vice President will not be accorded some of privileges his office is entitled to including his security,” said…

 • Govt engages Parliamentarians on forestry act amendment

  By Faith Mwafulirwa The Minister of Forestry and Natural Resources Nancy Tembo has urged members of parliament to support the forestry Act Amendment 2020 once brought in parliament for revision in order for the ministry to effectively implement the act. The minister was speaking in Lilongwe during an interface meeting she held with parliamentary committee…

 • AFAP DONATES FERTILIZER TO LESS PRIVILEGED – Mkusa commends the move

  The effects of COVID-19 have left footprints of poverty to many less privileged people and it is against this background that JF Investment through African Fertilizer and Agribusiness Partnership (afap) donated 100 bags of fertilizer from YALA worth over MWK2 million to elderly, disabled and very poor household farmers in Jean Sendeza’s constituency in Lilongwe….

 • Nankhumwa forming new party

  The Leader of Opposition in Parliament, Kondwani Nankhumwa is planning on forming a new party after falling out with some Democratic Progressive Party’s (DPP) senior members. Speaking to Afriem, a member of the Nankhumwa camp said that the new party will be stronger than the current DPP. “They are fabricating lies that Nankhumwa uses a…

css.php